48 Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aiche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.
49 Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;
50 naphe mbalame imodzi m'mbale yadothi, pamwamba pa madzi oyenda;
51 natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, nazibviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;
52 nayeretsenyumbandi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.
53 Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aicitire coitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.
54 Ici ndi cilamulo ca nthenda iri yonse yakhate, ndi yamfundu;