4 osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti aipereke copereka ca Yehova, ku bwalo la kacisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wocimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace;
5 kotero kuti ana a Israyeli azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.
6 Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la cihema cokomanako, natenthe mafuta akhale pfungo lokoma lokwera kwa Yehova.
7 Ndipo asamapheranso ziwanda nsembe zao, zimene azitsata ndi cigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.
8 Ndipo uzinena nao, Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,
9 osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.
10 Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.