7 Ndipo asamapheranso ziwanda nsembe zao, zimene azitsata ndi cigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.
8 Ndipo uzinena nao, Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,
9 osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.
10 Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.
11 Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, ucite cotetezera moyo wanu; pakuti wocita cotetezera ndiwo mwazi, cifukwa ca moyo wace.
12 Cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo ali yense wakugoneramwa inu asamadya mwazi.
13 Ndipo munthu ali yense wa ana a Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wace naufotsere ndi dothi.