5 Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'ciwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda cotupitsa, wosanganiza ndi mafuta.
6 Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.
7 Ndipo copereka cako cikakhala nsembe yaufa ya mumphika, cikhale ca ufa wosalala ndi mafuta.
8 Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera naco kwa wansembe, iyeyo apite naco ku guwa la nsembe.
9 Ndipo wansembeyo atengeko cikumbutso pa nsembe yaufa, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndico nsembe yamoto ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
10 Ndipo cotsalira ca nsembe yaufa cikhale ca Aroni ndi ana ace; ndico copatulikitsa ca nsembe zamoto za Yehova.
11 Nsembe iri yonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi cotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yacotupitsa, kapena yauci.