4 Munthu ali yense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo ali yense wokhudza cinthu codetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
5 ndi ali yense wokhudza cinthu cokwawa cakudetsedwa naco, kapenanso munthu amene akamdetsa naco, codetsa cace ciri conse;
6 munthu wokhudza ciri conse cotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lace ndi madzi.
7 Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pace adyeko zoyerazo, popeza ndizo cakudya cace.
8 Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.
9 Potero asunge cilangizo canga, angasenzepo ucimo, ndi kufera m'mwemo, pakuciipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo,
10 Mlendo asadyeko copatulikaco; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa nchito, asadyeko copatulikaco.