15 Ndipo unene ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Ali yense wotemberera Mulungu wace azisenza kucimwa kwace.
16 Ndi iye wakucitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akacitira dzina la Yehova mwano, awaphe.
17 Munthu akakantha munthu mnzace ali yense kuti afe, amuphe ndithu.
18 Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere yina; moyo kulipa moyo.
19 Munthu akacititsa mnansi wace cirema, monga umo anacitira momwemo amcitire iye;
20 kutyola kulipa kutyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anacitira munthu cirema, momwemo amcitire iye.
21 Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere yina; iye wakupha munthu, amuphe.