3 Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita;
4 ndidzakupatsani mvula m'nyengo zace, ndi dziko lidzapereka zipatso zace, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zace.
5 Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yochera mphesa, ndi nyengo yochera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta naco cakudya canu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.
6 Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zirombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.
7 Mudzapitikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga,
8 Asanu ainu adzapitikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapitikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.
9 Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukucurukitsani; ndipo ndidzakhazika cipangano canga ndinapangana nanuco.