41 Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzicepetsa, ndipo abvomereza kulanga kwa mphulupulu zao;
42 pamenepo ndidzakumbukila pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isake, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukila; ndipo ndidzakumbukila dzikoli.
43 Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ace, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzabvomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.
44 Ndiponso pali icinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kutyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Muhmgu wao.
45 Koma cifukwa ca iwo ndidzawakumbukila pangano la makolo ao, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.
46 Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa iye ndi ana a Israyeli m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.