6 Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zirombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.
7 Mudzapitikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga,
8 Asanu ainu adzapitikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapitikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.
9 Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukucurukitsani; ndipo ndidzakhazika cipangano canga ndinapangana nanuco.
10 Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kuturutsa zakale cifukwa ca zatsopano.
11 Ndidzamanga kacisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.
12 Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.