1 Ndipo copereka cace cikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema pamaso pa Yehova.
2 Ndipo aike dzanja lace pa mutu wa copereka cace, ndi kuipha pa cipata ca cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
3 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
4 ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.
5 Ndipo ana a Aroni azitenthe pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, iri pa nkhuni zimene ziri pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.