17 Koma ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi nyama yace, ndi cipwidza cace, anazitentha ndi mote kunja kwa cigono; monga Yehova adamuuza Mose.
18 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.
19 Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
20 Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zace; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.
21 Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
22 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.
23 Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wace naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa cala cacikuru ca ku dzanja lamanja lace, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja.