4 Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale colowa ca mapfuko anu, kuyambira ku Yordano, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa.
5 Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapitikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwacotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale colowa canu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.
6 Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kucita zonse zolembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, osacipambukira kulamanja kapena kulamanzere;
7 osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kuchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;
8 koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munacita mpaka lero lino.
9 Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikuru ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.
10 Munthu mmodzi wa inu adzapitikitsa anthu cikwi cimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.