17 Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babulo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babulo kufikira kwa Kristu mibadwo khumi ndi inai.
18 Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.
19 Koma Yosefe, mwamuna wace, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri,
20 Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.
21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao.
22 Ndipo zonsezi zinakhala kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
23 Onani namwali adzaima,Nadzabala mwana wamwamuna,Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli;ndilo losandulika, Mulungu nafe.