25 Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine.
26 Ndipo Iye anayankha, nati, Sicabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagaru.
27 Koma iye anati, Etu, Ambuye, pakutinso tiagaru timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.
28 Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, cikhulupiriro cako ndi cacikuru; cikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wace anacira nthawi yomweyo.
29 Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.
30 Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ace: ndipo Iye anawaciritsa;
31 kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nacira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.