1 Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anacokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano.
2 Ndipo makamu akuru a anthu anamtsata; ndipo Iye anawaciritsa kumeneko.
3 Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace pa cifukwa ciri conse?
4 Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu paciyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,
5 nati, Cifukwa ca ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?
6 cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Cifukwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.
7 Iwo ananena kwa Iye, Nanga cifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa cilekaniro, ndi kumcotsa?