13 Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ace pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.
14 Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: cifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.
15 Ndipo Iye anaika manja ace pa ito, nacokapo.
16 Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, cabwino nciti ndicicite, kuti ndikhale nao mayo wosatha?
17 Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za cinthu cabwino? alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
18 Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usacite cigololo, Usabe, Usacite umboni wonama,
19 Lemekeza atate wako ndi amako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.