11 Ndipo pofika ku nyumba anaona kamwanako ndi Mariya amace, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula cuma cao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.
12 Ndipo iwo, pocenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anacoka kupita ku dziko lao pa njira yina.
13 Ndipo pamene iwo anacoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amace, nuthawire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.
14 Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amace usiku, nacoka kupita ku Aigupto;
15 nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti,Ndinaitana Mwana wanga aturuke m'Aigupto.
16 Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'miraga yace yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
17 Pomwepo cinacitidwa conenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,