15 Sikuloleka kwa ine kodi kucita cimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi cifukwa ine ndiri wabwino?
16 Comweco omarizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omarizira.
17 Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khurni ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,
18 Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,
19 nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpacika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lacitatu.
20 Pomwepo anadza kwa Iye amace a ana a Zebedayo ndi ana ace omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.
21 Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna ciani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lao manja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.