22 Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa cimene mupempha, Kodi mukhoza kumwera cikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.
23 Iye ananena kwa iwo, Cikho canga mudzamweradi; koma kukhala ku dzanja lamanja kwangandi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.
24 Ndipo m'mene khurniwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.
25 Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akuru ao amacita ufumu pa iwo.
26 Sikudzakhala comweco kwa inu ai; koma amene ali yense akafuna kukhala warnkuru mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
27 ndipo amene ali yense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:
28 monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri.