5 Ndiponso anaturuka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nacita cimodzimodzi.
6 Ndipo poyandikira madzulo anaturuka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse cabe?
7 Iwo ananena kwa iye, Cifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso ku mundawo wampesa.
8 Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wace, Kaitane anchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omarizira kufikira kwa oyamba.
9 Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu ali yense rupiya latheka limodzi.
10 Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka.
11 Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,