1 Ndipo Yesn anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati,
2 Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wace phwando la ukwati,
3 natumiza akapolo ace kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.
4 Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsya: idzani kuukwati.
5 Koma iwo ananyalanyaza, nacoka, wina ku munda wace, wina ku malonda ace:
6 ndipo otsala anagwira akapolo ace, nawacitira cipongwe, nawapha.
7 Koma mfumu inakwiya; nituma asilikari ace napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.