13 Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye ku mdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
14 Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.
15 Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwace.
16 Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu ali yense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.
17 Cifuka cace mutiuze ife, muganiza ciani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
18 Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?
19 Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka.