17 Cifuka cace mutiuze ife, muganiza ciani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
18 Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?
19 Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka.
20 Ndipo Iye anati kwa iwo, Nca yani cithunzithunzi ici, ndi kulemba kwace?
21 Nanena iwo, Ca Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace patsani kwa Kaisara zace za Kaisara, ndi kwa Mulungu zace za Mulungu.
22 Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nacokapo.
23 Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye,