24 Ndipo uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza;
25 ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: onani, siyi yanu.
26 Koma mbuye wace anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza;
27 cifukwa cace ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lace.
28 Cifukwa cace cotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.
29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zocuruka: koma kwa iye amene alibe, kudzacotsedwa, cingakhale cimene anali naco.
30 Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pace ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.