4 nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi cinyengo, namuphe.
5 Koma ananena iwo, Pa dzuwa la cakudya iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.
6 Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,
7 anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa yaalabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatari, nawatsanulira pamutu pace, m'mene Iye analikukhala pacakudya.
8 Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Cifukwa ninji kuononga kumeneku?
9 Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi.
10 Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? popeza andicitira Ine nchito yabwino.