9 Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi.
10 Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? popeza andicitira Ine nchito yabwino.
11 Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.
12 Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandicitiratu ici pa kuikidwa kwanga.
13 Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ici cimene mkaziyo anacitaci cidzakambidwanso cikumbukiro cace.
14 Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lace Yudase Isikariote, anamuka kwa ansembe akuru,
15 nati, Mufuna kundipatsa ciani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.