1 Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kumka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.
2 Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pace anamva njala.
3 Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.
4 Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa,Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akuturuka m'kamwa mwa Mulungu.