11 Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.
12 Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;
13 ndipo anacoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao ira pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafitali:
14 kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,
15 It Dziko la Zebuloni ndi dziko la N afitali,Njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano,Galileya la anthu akunja,
16 Anthu akukhala mumdimaAdaona kuwala kwakukuru,Ndi kwa iwo okhala m'malo mthunzi wa imfa,Kuwala kunaturukira iwo.
17 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.