16 Anthu akukhala mumdimaAdaona kuwala kwakukuru,Ndi kwa iwo okhala m'malo mthunzi wa imfa,Kuwala kunaturukira iwo.
17 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
18 Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya, mbale wace, analikuponya psasa m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.
19 Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.
20 Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.
21 Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.
22 Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.