8 Pomwenso mdierekezi anamuka naye ku phiri lalitari, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;
9 nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.
10 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa,Ambuye Mulungu wako udzamgwadira,Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.
11 Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.
12 Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;
13 ndipo anacoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao ira pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafitali:
14 kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,