10 Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
11 Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.
12 Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
13 Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14 Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.
15 Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali m'nyumbamo.
16 Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.