12 Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
13 Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14 Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.
15 Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali m'nyumbamo.
16 Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
17 Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.
18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.