23 Cifukwa cace ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,
24 usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nucoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.
25 Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.
26 Indetu ndinena ndi iwe, sudzaturukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumariza ndiko.
27 Munamva kuti kunanenedwa, Usacite cigololo;
28 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kucita naye cigololo mumtima mwace.
29 Koma 1 ngati diso lake lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'gehena.