20 Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wace.
21 Ndipo wina wa ophunzira ace anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga.
22 Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.
23 Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ace anamtsata Iye.
24 Ndipo onani, m panauka namondwe wamkuru panyanja, kotero kuti ngalawa inapfundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo.
25 Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tirikutayika.
26 Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikuru.