34 Koma Afarisi analinkunena, Aturutsa ziwanda ndi mphamvu zace za mfumu ya ziwanda.
35 Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, naciritsa nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.
36 Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi cisoni cifukwa ca iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
37 Pomwepo ananena kwa ophunzira ace, Zotuta zicurukadi koma anchito ali owerengeka.
38 Cifukwa cace pempherani Mwini zotuta kuti akokose anchito kukututakwace.