5 pakuti capafupi nciti, kunena, Macimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka nuyende?
6 Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira macimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge chika lako, numuke kunyumba kwako.
7 Ndipo ananyamuka, napita ku nyumba kwace.
8 Ndipo m'mene anthu a makamu anaciona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
9 Ndipo Yesu popita, kucokera kumeneko, anaona munthu, dzina lace Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
10 Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pacakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ocimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace.
11 Ndipo Afarisi, pakuona ici, ananena kwa ophunzira ace, Cifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ocimwa?