7 Ndipo ananyamuka, napita ku nyumba kwace.
8 Ndipo m'mene anthu a makamu anaciona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
9 Ndipo Yesu popita, kucokera kumeneko, anaona munthu, dzina lace Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
10 Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pacakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ocimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace.
11 Ndipo Afarisi, pakuona ici, ananena kwa ophunzira ace, Cifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ocimwa?
12 Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala.
13 Koma mukani muphunzire nciani ici:Ndifuna cifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa.