1 NDIPO atamwalira Ahabu, Moabu anapandukana ndi Israyeli.
2 Ndipo Ahaziya anagwa kubzola ku made wa cipinda cace cosanja cinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni ngati ndidzacira nthenda iyi.
3 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti mukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni?
4 Cifukwa cace atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nacoka Eliya.
5 Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera cifukwa ninji?
6 Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.