15 Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mibvi; nadzitengera uta ndi mibvi.
16 Nati kwa mfumu ya Israyeli, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ace pa manja a mfumu.
17 Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Mubvi wa cipulumutso wa Yehova ndiwo mubvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha.
18 Nati iye, Tengani mibvi; naitenga, Nati kwa mfumu ya Israyeli, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.
19 Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.
20 Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amoabu analowa m'dziko poyambira caka.
21 Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima ciriri.