3 Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asuri kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.
4 Koma mfumu ya Asuri anampeza Hoseya alikucita ciwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Aigupto, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asuri, monga akacita caka ndi caka; cifukwa cace mfumu ya Asuri anamtsekera, nammanga m'kaidi.
5 Pamenepo mfumu ya Asuri anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.
6 Caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Asuri analanda Samariya, natenga Aisrayeli andende, kumka nao ku Asuri; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.
7 Kudatero, popeza ana a Israyeli adacimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwaturutsa m'dziko la Aigupto pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, ndipo anaopa milungu yina,
8 nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli, ndi m'miyambo ya mafumu a Israyeli imene iwo anawalangiza.
9 Ndipo ana a Israyeli anacita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse ku nsanja ya olonda ndi ku mudzi walinga komwe.