12 cifukwa cace atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda coipa, cakuti yense acimvera cidzamliritsa mwini khutu.
13 Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu cingwe coongolera ca Samariya, ndi cingwe colungamitsira ciriri ca nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuibvundikira.
14 Ndipo ndidzataya cotsala ca colowa canga, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo cakudya ndi cofunkha ca adani ao onse;
15 popeza anacita coipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga citurukire makolo ao m'Aigupto, mpaka lero lino.
16 Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.
17 Macitidwe ena tsono a Manase, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
18 Nagona Manase ndi makolo ace, naikidwa m'munda wa nyumba yace, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwace Amoni mwana wace.