1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
2 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lace, osapambukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.
3 Ndipo kunali caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, ku nyumba ya Yehova, ndi kuti,
4 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;