1 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a m'Yerusalemu.
2 Nikwera mfumu kumka ku nyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi nave, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la cipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.
3 Niima mfumu paciunda, nicita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a cipangano colembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.
4 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo laciwiri, ndi olindira pakhomo, aturutse m'Kacisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi cifanizo cija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lace kumka nalo ku Beteli.
5 Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; wo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.