10 Ndi khamu lonse la Akasidi linali ndi mkuru wa olindirira linagumula linga la Yerusalemu louzinga.
11 Ndi anthu otsalira m'mudzi, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babulo, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkuru wa olindirira anamuka nao andende.
12 Koma mkuru wa olindirira anasiya osaukadi a m'dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi,
13 Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ace, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazithyolathyola, natenga mkuwa wace kumka nao ku Babulo.
14 Nacotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.
15 Ndi zoparira moto, ndi mbale zowazira za golidi yekha yekha, ndi zasiliva yekha yekha, mkuru wa asilikari anazicotsa.
16 Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomo, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoza kuyesa kulemera kwace.