1 Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israyeli m'Samariya m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.
2 Nacita coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wace ndi amace; pakuti anacotsa coimiritsa ca Baala adacipanga atate wace.
3 Koma anakangamira zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene anacimwitsa nazo Israyeli, osalekana nazo.
4 Ndipo Mesa mfumu ya Moabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israyeli ubweya wa ana a nkhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.