1 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anapfuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ace.
2 Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikucitire ciani? undiuze m'nyumba mwako muli ciani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.
3 Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.
4 Nulowe, uudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.
5 Pamenepo anamcokera, nadzitsekera yekha ndi ana ace amuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.