14 Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa cuma, popeza wamcepetsa.
15 Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;
16 pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ace amuna cuma cace, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.
17 Koma azibvomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lace la zace zonse; popeza iye ndiye ciyambi ca mphamvu yace; zoyenera woyamba kubadwa nzace.
18 Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wace, kapena mau a mai wace, wosawamvera angakhale anamlanga;
19 azimgwira atate wace ndi mai wace, ndi kuturukira naye kwa akuru a mudzi wace, ndi ku cipata ca malo ace;
20 ndipo anene kwa akulu a mudzi wace, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.