13 Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
14 Ndipo copereka cace ca kwa Yehova cikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera naco copereka cace cikhale ca njiwa, kapena ca maunda.
15 Ndipo wansembe abwere naco ku guwa la nsembe, namwetule mutu wace, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wace aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,
16 nacotse citsokomero, ndi cipwidza cace, nazitaye kufupi kwa guwa la nsembe, kum'mawa, kudzala;
17 nang'ambe mapiko ace osawacotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni ziri pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.