9 koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
10 Ndipo copereka cace cikakhala ca nkhosa, kapena ca mbuzi, cikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda cirema.
11 Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
12 Ndipo aikadzule ziwalo zace, pamodzi ndi mutu wace ndi mafuta ace; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni ziri pa mota wa pa guwa la nsembe.
13 Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
14 Ndipo copereka cace ca kwa Yehova cikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera naco copereka cace cikhale ca njiwa, kapena ca maunda.
15 Ndipo wansembe abwere naco ku guwa la nsembe, namwetule mutu wace, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wace aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,