1 MIYAMBI ya Solomo mwana wa Davide, mfumu ya Israyeli.
2 Kudziwa nzeru ndi mwambo;Kuzindikira mau ozindikiritsa;
3 Kulandira mwambo wakusamalira macitidwe,Cilungamo, ciweruzo ndi zolunjika;
4 Kucenjeza acibwana,Kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;
5 Kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;Ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;
6 Kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lace,Mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.